Matthew 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idaŵatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza niima pamwamba pomwe panali kamwanako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza niima pamwamba pomwe panali kamwanako.