Matthew 20:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaalaŵirira m'mamaŵa kukalemba anthu okagwira ntchito m'munda wake wamphesa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anaturuka mamawa kuka lembera anchito a m'munda wace wampesa.