Matthew 20:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adati, ‘Aa! Anzathu otsiriziraŵa angogwira ntchito kanthaŵi pang'ono, bwanji mwaŵapatsa malipiro olingana ndi athu, pamene ifeyo tathyoka nayo ntchito tsiku lathunthu, ndi chidzuŵa chonse chija?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Omarizira awa anagwira nchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi: kutentha kwace.