Matthew 20:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tenga malipiro ako, uzipita. Mwiniwakene ndafuna kuti ndipatse wolembedwa potsirizayu molingana ndi iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womarizira monga kwa iwe.