Matthew 20:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpacika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lacitatu.