Matthew 20:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yesu adati, “Chabwino, mudzamwa nao chikho changacho. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Atate ndiwo adzapereke malo ameneŵa kwa amene Atatewo adaŵakonzera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye ananena kwa iwo, Cikho canga mudzamweradi; koma kukhala ku dzanja lamanja kwangandi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.