Matthew 20:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la anthu ambiri.