Matthew 20:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adaŵazazira akhunguwo kuti akhale chete. Koma iwo nkumafuulirafuulira kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, muticitire cifundo, Inu Mwana wa Davide.