Matthew 20:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pafupi 5 koloko madzulo adapitanso nakapeza enanso akungokhala. Adaŵafunsa kuti, ‘Bwanji mwangokhala khale pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo poyandikira madzulo anaturuka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse cabe?