Matthew 20:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Dzuŵa likuloŵa, mwinimunda uja adauza kapitao wake kuti, ‘Kaŵaitane antchito aja, uŵalipire. Uyambire amene alembedwa potsirizawo, utsirizire oyamba aja.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wace, Kaitane anchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omarizira kufikira kwa oyamba.