Matthew 21:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaona zodabwitsa zimene Iye ankachita. Adamvanso ana akufuula m'Nyumba ya Mulungu kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide.” Ndiye iwowo adapsa nazo mtima,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ansembe akuru ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazicita, ndi ana alinkupfuula kuKacisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,