Matthew 21:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataona mkuyu pambali pa mseu, nkupitapo, sadapezepo chilichonse koma masamba okhaokha. Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya usadzabalenso konse zipatso.” Nthaŵi yomweyo mkuyu uja udachita kuti gwa, kuuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okha okha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso cipatso ku nthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.