Matthew 21:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti, “Kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene Iye analowa m'Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene Iye analowa m'Kacisi, ansembe akuru ndi akuru anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Mucita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?