Matthew 21:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzeni kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati muneliuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi: