Matthew 21:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi Yohane kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu?” Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono simudamkhulupirire?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzake, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?” Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ubatizo wa Yohane, ucokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzace, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?