Matthew 21:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi inu, mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵiri. Adapita kwa woyamba, nakamuuza kuti, ‘Mwana wanga, pita ukagwire ntchito m'munda wamphesa lero.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga mutani? Munthu anali cao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero nchito ku munda wampesa.