Matthew 21:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Yohane Mbatizi adaabwera nadzakuwonetsani njira ya chilungamo, inu osamkhulupirira, m'menemo okhometsa msonkho ndi akazi adama adamkhulupirira. Inuyo ngakhale mudaziwona zimenezo, simudasinthe maganizo pambuyo pake kuti muzimkhulupirira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvera iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalapa pambuyo pake, kuti mumvere iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya cilungamo, ndipo simunamveraiye; koma amisonkho ndi akazi aciwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munaciona, simunalapa pambuyo pace, kuti mumvere iye.