Matthew 21:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Imvani fanizo lina. Munthu wina anali ndi munda wake. M'mundamo adaabzalamo mipesa, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.