Matthew 21:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene alimiwo adaona mwana wakeyo, adayamba kuuzana kuti, ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzace, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga colowa cace.