Matthew 21:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi monga simudaŵerenge Malembo aja akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa. Ambuye ndiwo adachita zimenezi, ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenga konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti: “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana, womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya. Ambuye wachita izi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yesu ananena kwa iwo, 1 Kodi simunawerenga konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba Womwewu unakhala mutu wa pangondya: ici cinacokera kwa Ambuye, Ndipo ciri cozizwitsa m'maso mwathu?