Matthew 21:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uzani mzinda wa Ziyoni kuti, ‘Ona mfumu yako ikudza kwa iwe. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu. Zoonadi yakwera pa kabulu, mwana wa nyama yosenza katundu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uza mwana wamkazi wa Ziyoni, taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yofatsa ndi yokwera pa bulu, pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tauzani mwanawamkazi wa Ziyoni, Taona, Mfumu yako idza kwa iwe, Wofatsa ndi wokwera pa buru, Ndi pa kaburu, mwana wa nyama yonyarnula katundu.