Matthew 21:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ochuluka amene anali patsogolo, ndi amene anali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana m'Kumwambamwamba!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti, “Hosana Mwana wa Davide!” “Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!” “Hosana mmwambamwamba!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inapfuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana m'Kumwambamwamba!