Matthew 22:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamene mfumu ija idaloŵa m'nyumbamo kukaona anthu odzadya phwando aja, idapezamo wina amene sadavale chovala chaukwati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala cha ukwati;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosabvala cobvala ca ukwati;