Matthew 22:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kwathu kudaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, nkumwalira. Tsono popeza kuti analibe mwana, adasiyira mbale wake mkazi wake uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwake mkazi wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwace mkazi wace;