Matthew 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamenepo mfumu idapsa mtima kwambiri, mwakuti idatuma ankhondo ake kuti akaononge opha anzao aja, ndi kutentha mudzi wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu inakwiya; nituma asilikari ace napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao.