Matthew 23:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumayenda maulendo ambirimbiri pa nyanja ndi pa mtunda, kufunafuna ngakhale munthu mmodzi yekha kuti atembenuke ndi kusanduka wophunzira wanu. Tsono akapezeka, mumamsandutsa woyenera kulangidwa ku Gehena kuposa inu kaŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa Gehena woposa inu kawiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumayenda maulendo ambiri pa mtunda ndi pa nyanja kuti mutembenuze munthu mmodzi, ndipo akatembenuka, mumamusandutsa kukhala mwana wa gehena kawiri kuposa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri.