Matthew 23:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muli ndi tsoka, inu atsogoleri akhungu! Inu mumati, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, asunge lumbiro lakelo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu! Mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula Nyumba ya Mulungu, zilibe kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula ndalama zagolide za mʼNyumbayo, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene ali yense akalumbira kuchula Kacisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula golidi wa Kacisi, wadzimangirira.