Matthew 23:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumatinso, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali guwa lansembe, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali choperekedwa pa guwa, asunge lumbiro lakelo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula guwa lansembe, sizitanthauza kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula mphatso ya paguwa lansembe, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso, Amene ali yense akalumbira kuchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula mtulo wa pamwamba pace wadzimangirira.