Matthew 23:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Muli ngati manda opaka njeresa, amene amaoneka okongola kunja, pamene m'kati mwake m'modzaza ndi mafupa a anthu akufa ndi zoola zina zilizonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Muli ngati ziliza pa manda zowala kunja zimene zimaoneka zokongola koma mʼkatimo mwadzaza mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zina zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwace, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.