Matthew 23:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumakonza bwino manda a aneneri, ndipo mumakongoletsa ziliza za anthu olungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumamanga ziliza za aneneri ndi kukongoletsa manda a olungama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama,