Matthew 23:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake muzichita ndi kutsata zonse zimene iwo amakuphunzitsani. Komatu musamatsanzira zimene amachita, pakuti sachita zimene amaphunzitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zao; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho muziwamvera ndi kuchita chilichonse chimene akuwuzani. Koma musachite zimene amachita, popeza sachita zimene amaphunzitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace zinthu ziri zonse zimene iwo akauza inu, citani nimusunge; koma musatsanza nchito zao; pakuti iwo amalankhula, komasamacita.