Matthew 23:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mvetsetsani tsono! Ine ndidzakutumizirani aneneri, ndiponso anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena mudzaŵapha ndi kuŵapachika pa mtanda. Ena mudzaŵakwapula m'nyumba zanu za mapemphero, ndipo mudzaŵazunza pakuŵapirikitsa kuchokera ku mudzi wina mpaka ku mudzi wina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndi kutumizirani aneneri ndi anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena a iwo mudzawapha ndi kuwapachika; ena mudzawakwapula mʼmasunagoge anu ndi kuwafunafuna kuchokera mudzi wina kufikira wina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca ici, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapacika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kucokera ku mudzi umodzi, kufikira ku mudzi wina;