Matthew 23:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafuna ai!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ace m'mapiko ace, koma inu simunafuna ai!