Matthew 23:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo amamanga katundu wosautsa kunyamula nkusenzetsa anthu, koma iwowo samukhudzako mpang'ono pomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amamanga akatundu olemera nawayika pa mapewa a anthu, koma iwo eni safuna kuwanyamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi cala cao.