Matthew 23:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonse zimene amachita amangozichita kuti anthu aŵaone. Amadzimangirira timapukusi tikulutikulu ta mau a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono. Amatalikitsanso mphonje za zovala zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma amacita nchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa citando cace ca njirisi zao, nakulitsa mphonje,