Matthew 24:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo, akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma Mulungu adzaŵachepetsa masikuwo chifukwa cha anthu amene Iye adaŵasankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense: koma cifukwa ca osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.