Matthew 24:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yesu anakhala pansi pa phiri la Olivi, ophunzira ake anabwera kwa Iye mwamseri nati, “Tiwuzeni, kodi izi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi zizindikiro za kutha kwa dziko zidzakhala chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?