Matthew 24:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Yang'anani mkuyu kuti mutengerepo phunziro. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete, ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsopano kuchokera ku mtengo wamkuyu phunzirani ichi: Pamene uyamba kuphukira, masamba ake akatuluka, mumadziwa kuti dzinja layandikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene tsopano nthambi yace iri yanthete, nipuka masa-i mba ace, muzindikira kuti dzinja liyandikira;