Matthew 24:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma za tsiku ili ndi nthawi yake sadziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Palibe amene adziwa za tsikulo kapena nthawi, angakhale angelo akumwamba, angakhale Mwana, koma Atate okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma za tsiku ilo ndi nthawi yace sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.