Matthew 24:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, koma onetsetsani kuti musadzidzimuke nazo. Zotere ziyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.