Matthew 25:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adaloŵa naye pamodzi m'nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo, analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.