Matthew 25:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ace, napereka kwa iwo cuma cace.