Matthew 25:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, ndipo adzakhala nazo zochuluka. Aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zocuruka: koma kwa iye amene alibe, kudzacotsedwa, cingakhale cimene anali naco.