Matthew 25:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munacitira ici mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandicitira ici Ine.