Matthew 25:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo nawonso adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, kapena muli ndi ludzu, kapena wamaliseche, ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife osachitapo kanthu?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamarisece, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?