Matthew 26:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwinowu pa dziko lonse lapansi, azikafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indetu ndinena kwa inu, kumene kulikonse Uthenga uwu Wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ici cimene mkaziyo anacitaci cidzakambidwanso cikumbukiro cace.