Matthew 26:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adaŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, ‘Aphunzitsi akuti nthaŵi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Paska pamodzi ndi ophunzira ao.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Pitani mu mzinda kwa munthu wakutiwakuti ndipo kamuwuzeni kuti, ‘Aphunzitsi akuti, nthawi yanga yoyikidwa yayandikira. Ine ndidzadya phwando la Paska ndi ophunzira anga ku nyumba kwako.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena. Nthawi yanga yayandikirai ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.