Matthew 26:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wa Munthu adzaphedwa monga mmene kunalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene apereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwana wa munthu acokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.