Matthew 26:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, “Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yace pansi, napemphera, nati, Atate, ngati nkutheka, cikho ici cindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma lou.