Matthew 26:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu akulankhula choncho, wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye ali cilankhulire, onani, Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikuru la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kucokera kwa ansembe akuru ndi akuru a anthu.